Selena Gomez, katswiri woyimba nyimbo zachikondi komanso wosewera mafilimu padziko lonse, tsopano wakwatirana ndi woyimba nyimbo Benny Blanco pa 27 September 2025 ku Santa Barbara, California.
Ukwatiwu unali wosangalasa, komanso kunabwera anthu odziwika, ndipo unali ngati nyimbo ya chikondi yomwe imayenda m’mitu ya atolankhani kuyambira pamene awiriwa anavomereza za chibwenzi chawo kugulu mu 2023.

Gomez anachititsa chidwi alendo ndi velo lake lapamwamba la Ralph Lauren, lomwe linali lokongola, lokhala ndi mphumi ya maluwa komanso lopangidwa mwadongosolo, lomwe linagwirizana ndi thupi lake kusonyeza kukongola kosatha. Blanco, naye, anavala zovala za Ralph Lauren, zosonyeza kufanana kwa chikondi chawo. Wopanga zovalayu, amene nthawi zambiri amasamalira zovala za ukwati wa anthu wotchuka, anali nawo pa mwambowu.

Chimodzi mwa zinthu zopatsa chidwi pa mwambowu unali mphete ya Blanco yopangidwa ndi golide wolemera 18 carats, yosindikizidwa mkati ndi tsiku la ukwati wawo. Mpheteyo inalinso ndi miyala ya ruby ndi aquamarine, chizindikiro cha mwezi wobadwa wa onse awiri, zomwe zinapangitsa mpheteyo kukhala ndi tanthauzo lachinsinsi komanso lachikondi.
Mndandanda wa alendo unali wosakanikirana ndi abale, abwenzi apamtima komanso akatswiri ambiri woyimba nyimbo ndi kupanga mafilimu.
Malo a ku Santa Barbara anapereka chithunzithunzi chokongola, ndi nyanja ndi maluwa okongoletsa omwe anagwirizana bwino ndi kapangidwe ka velo la Serena Gomez.

Awiriwa anavomereza za chibwenzi chawo mu December 2024, patatha chaka chimodzi akupanga chibwenzi chomwe chinali cha chinsinsi. Ulendo wawo kuchokera kugwira ntchito limodzi mu nyimbo kufika pokwatirana wakhala nkhani yosangalatsa kwa okonda nyimbo zawo komanso ma filimu awo padziko lonse lapansi.
Leave a Reply