Save 20% off! Join our newsletter and get 20% off right away!

Osawonesa Chitupa Cha Salary Asamwe, Awumvere Fungo

Boma la Saudi Arabia tsopano lafewetsa lamulo lokhwima lokhudza kugulitsa mowa, polola anthu obwera mu dzikolo komanso omwe si Asilamu ndipo amalandira malipiro oposa 50,000 riyal (pafupifupi $13,300) pa mwezi kuti atha kumagula mowa mwalamulo. Malinga ndi zomwe boma lanena, anthu ofuna kugula bibida aziyenera kuwonetsa chiphaso cha malipiro awo kuti aloledwe kulowa mu sitolo yokhayo ya mowa yomwe ilipo mdzikolo.

Izi zikuwonetsa gawo lina la kusintha kwa chikhalidwe m’dziko la Saudi Arabia mkati mwa pulani ya Vision 2030, yomwe cholinga chake ndi kukopa akatswiri ochokera kunja ndi kupitisa patsogolo mbiri ya dzikolo padziko lonse.

Ngakhale kugulitsa ndi kumwa mowa kukadali koletsedwa kwa nzika za Saudi komanso kwa Asilamu onse, lamulo latsopanoli likupatsa alendo omwe si achipembezo Cha chisilamu omwe amalandira malipiro okwera mwayi wogula mowa m’njira yololezedwa ndi boma.

Boma silinatsimikizire ngati kusinthaku kukhoza kufalikira ku masitolo ena kapena kuwonjeza anthu olandirapo, koma akatswiri ati iyi ndi njira imodzi yochepetsera malamulo okhwima kuti dzikolo lizintha kukopa alendo komanso aluso ochokera kunja.

Komabe, chilango chokhwima chokhudzana ndi kusunga mowa mosaloledwa, kumwa pagulu, kapena kugulitsa kwa ena chikadali chomwecho, kuwonetsa kuti ngakhale pali kusintha, dzikoli likadali pa njira yosamala kwambiri pophatikiza kusintha ndi chikhalidwe chake chokhazikika.