Mzimayi amene adaba mwana wina ku Chirimba wagwidwa lero ku m’mawa ku Lunzu ndi mwanayo atamuveka dzovala zina.
Atakwenyedwa nkufunsidwa kuti anabelanji mwanayo akusintha sintha ma statement ndipo poyilumikiza nkhani, zikuoneka kuti mayiyu adakhalapo ndi mimba ndipo adapanga miscarriage.
Koma atapanga miscarriage sadamuwuze mamuna wake amene amakhala kutali moti adamunamiza kuti mwanayo wabadwadi. Ndiye iyeyo adaba mwanayo ndicholinga choti adzakamuonetse mamunayo kuti mwana uja ndi uyu ncholinga choti adzipeleka chithandizo.
Atafika kwa mamunayo adafotokoza kuti anawo adabadwa mapasa ndipo m’modzi adamwalila ndipo adatsalayu amangomumwetsa enjoy ndipo samuyamwitsa popeza zimamupatsa maganizo a winayo akati amuyamwitse.
Pakadali pano mayiyu wamangidwa ndipo ali ku chirimba police pamodzi ndi mamuna wakeyo ndipo apolisi akufufuzabe nkhaniyi komanso kumupana ndimafunso popeza sakukhutitsidwa ndi zimene akufotokoza mayiyu
Leave a Reply