Save 20% off! Join our newsletter and get 20% off right away!

MNENERI ‘WONYENGA’ KHOSA ZAKE WAPEZEKA OLAKWA PA MILANDU 17

Mtumiki wa Mulungu wopuma yemwe amamuganizila kuti amachitira nkhanza zachigololo khosa zamu mpingo womwe zochitika zake zinali zodabwitsa wotchedwa Nine O’clock Service (NOS), amupeza olakwa pa milandu 17 yomwe anawachitira amayi asanu ndi anayi(9) amu mpingo wake.

M’busayu yemwe dzina lake ndi Chris Brain ndipo ali ndi dzaka 69, anali mtsogoleri wa mpingo wa NOS womwe unali wodziwika bwino chama 1980’s mpaka ma 90’s mu dera la Sheffield mu dziko la mangalande.

Chris Brain, Mtumiki wopuma wa mpingo wa Nine O’clock Service yemwe amanyenga khosa zake.

Brain amaganizilidwa kuti adapalamula milanduyi mu dzaka zomwe anali mtsogoleri wa mpingowu ndipo wapezeka olakwa potsatira chigamulo cha bwalo la milandu la “Inner London Crown”.

Mtumikiyi sanapezeke olakwa pa milandu ina khumi ndi isanu(15) yochita m’khalidwe wosayenera kwa amayi ndipo oweluza milandu adakali mkati mokambilana za milandu ina inayi(4) la m’khalidwe wosayenera komanso umodzi wogwililira.

Pa mlanduwu, nthumwi ya mbali ya boma a Tim Clark adati amayi ena anazuzidwa mwa chigololo pamene amapephera mu mpingowu ndipo adasakhidwa kupita ku “Homebase” komwe amayenera kumagwira ntchito mu nyumba ya mtumikiyo komanso kumawasamalira pamodzi ndi banja lawo(mkazi wawo ndi mwana wa mkazi).

Malingana ndi umboni wa anthu omwe amaona zomwe zimachitika, amayiwa amawuzidwa kuti avale zovala za chikoka za m’kati(Lingerie) pogwira ntchito komanso nthawi zina amamuzungulira uku akumugwiragwira m’thupi mwachigololo kenako amayenera agonane naye nthawi yogona ikakwana.

Ngakhale mtumikiyu amakana milanduyi mu khothi pamene amazengedwa milanduyi, iyeyu adali atavomera kale kuchita zadama komanso zosayenera ndi khosa zake mu pulogalamu yakafukufuku ya kanema ku BBC mu chaka cha 1995.

Mtumikiyu adatula udindo wake ngati mtsogoleri wa mpingowu kanema waku BBC yu asadawulutsidwe mu chaka cha 1996 ndipo mpingowo udathesedwa potsatira ma report oti mtumikiyu akuchita m’khalidwe wosayenera komanso kusagwilisa bwino ntchito mphamvu zake ngati otsogolera mpingowo.

Padakali pano akuyembekezera chigamulo.

Source: BBC News