Moto wawononga ma nyumba amabanja angapo ku mudzi wa Natirae, m’boma la Nabilatuk kumpoto kwa Uganda, pamene ena amasaka mbewa. Motowu unayambitsidwa pa nthawi yosaka mbewa ndipo unafalikira msanga chifukwa cha nyumba l zomangidwa za maudzu zomwe zimakhala zouma komanso zoyaka mosavuta.
Malinga ndi lipoti la Uganda Red Cross Society (URCS), manyumba asanu ndi awiri awonongeka kwathunthu, ndipo mabanja ambiri tsopano alibe pokhala. Anthu ataya nyumba zawo, zinthu zofunika komanso chakudya chonse m’phindi zochepa pamene moto unawotcha midzi yonse.
Pambuyo pa ngoziyi, bungwe la URCS linatumiza gulu ku mudzi wa Natirae kuti likawunike mulingo wa kuwonongeka komwe kwachitika ndiponso kupereka chithandizo chadzidzidzi kwa mabanja ovutika. Ntchitoyi ndi yopereka thandizo mwachangu komanso kuzindikira zosowa zomwe zikufunika kwambiri pamudzipa.
M’mawu awo, URCS idatsimikizira mgwirizano wake ndi akuluakulu am’dziko komanso atsogoleri a m’mudzi kuti achulukitse maphunziro okhudza ngozi za moto. Iwo anatsindika kufunika kogwiritsa ntchito njira zotetezera moto makamaka m’madera omwe miyambo kapena zochita zatsiku ndi tsiku zimatha kuika anthu pachiwopsezo.
Bungweli linanenanso kuti pali kufunika kolimbitsa malamulo ndi njira zotetezera moto kuti ateteze moyo ndi katundu, chifukwa zochitika ngati izi—ngakhale zotheka kupewa—zikupitilira kusonyeza momwe anthu okhala m’ma nyumba omwe amayaka mosavuta ali pachiwopsezo.










Leave a Reply