Kafukufuku watsopano wa a katswiri ozama pa nkhani za science akuwonesa kuti apeza njira yomwe angathe kudziwila maganizo a anthu.

Izi dzaziwika potsatira kafukufuku yemwe amapanga pofuna kupeza njira yothandizira kudziwa zomwe anthu omwe ali ndi ulumari okanika kuyakhula akufuna kunena pogwirisa ntchito makina a magesi.
Zotsatirazi zaza patatha makumi dzikwi akupanga kafukufukuyi kuti athandizire anthu a ulumali osayakhula (mute) komanso omwe amavutika kuyakhula potsatira kudwala matenda a zazi pakhosi(stroke) kapena Amyothroplic Lateral Sclerosis (A.L.S) omwe amafowora minofu ya malo omwe amathandizira kutulusa mawu.
Akatswirawa anayesa njira yoika ma electrodes onwe amagwira ntchito yonyamula yotathauzira nyesi zamu ubongo kapena kuti ma uthenga ochokera ku ubongo ndikuwatathauzira ngati mawu.
Kudzera mu njirayi akatswiriwa adakwanirisa kutathauzira ma signal omwe ubongo umatumiza pamene munthu akufuna kuyakhula kukhala mawu.
Padakali pano zikuonesatso kuti kudzera mu njira yomweyi, akatswiriwa akwanilitsaso kutathauzira maganizo a munthu kuti azikhala mawu. Izi zikutathauza kuti tsopano kudzera mu njirayi anthu azikwanirisa kudziwa maganizo a munthu wina zomwe zinali zosatheka.
Source: New York Times
Leave a Reply