Bungwe la Lagos State Internal Revenue Service (LIRS) lasindikiza za kutsekedwa kwa sitolo ya Shoprite yomwe ili ku Ikeja City Mall, litati kampaniyo yalephera kutsatira malamulo ake okhudza kulipira misonkho. Malinga ndi LIRS, kutsekedwa kumeneku ndi gawo la kampeni yolimbikitsa kuti mabizinesi onse omwe amagwira ntchito mu mzinda wa Lagos azilipira misonkho moyenera.
Kutsekedwaku kwachitika lero ndipo kwadabwitsa ogula komanso okhalamo omwe nthawi zambiri amapita ku malo ogulitsirawo. A LIRS ati akhala atumiza mawuthenga owachenjeza kangapo kwa oyang’anira sitolo ya Shoprite koma sanatsatire zomwe amalamulidwa.
Pomwe LIRS lati zomwe apangazi ndi zovomerezeka komanso yachizolowezi pa ntchito zawo zowona kuti ndondomeko ya mmisonkho ikutsatilidwa. Padakali pano anthu ambiri akudikirira kuona zomwe Shoprite iyankhe pa zomwe ikuwaganizirazi. Sitoloyo ikhala yotsekedwa mpaka kampaniyo itakhazikitsa malamulo onse ndikutsimikizira kutsatira kwake kwa misonkho.










Leave a Reply