Save 20% off! Join our newsletter and get 20% off right away!

KALAWE WADABWA NAYE SPANNER MALAWI

Pamene Spanner Malawi wakwanilitsa kupambana mpikisano wokudya zakudya zosiyanasiyana womwe unachitikira mu mzinda wa Lagos m’dziko la Nigeria woyimba chamba cha Hip-Hop Kalawe wadabwa naye Spanner Malawi.

Spanner Malawi in action.

Kalawe yemwe m’modzi mwa oyimba odziwika m’Malawi muno wati sakuntha kumvetsa kuti zakudya zomwe amadya Spanner zimapita kuti popeza Spanner si onenepa kapena Chiphona( monga mmene zimayenera kukhala munthu ukamadya kwambiri).

Woyimbayu walemba pa tsamba lake la mchezo pa Facebook kuti mmene amadyera Spanner Malawi amayenera kukhala onenepa kwambiri kapena ngati amanyamula zitsulo kuti asanenepe amayenera kukhala chiphona koma ndizodabwitsa kuti Spanner si onenepa, kanthupi kali gwaa komanso si chi panza. Nde funso ndilokuti phax yomwe amadyayo imapita kuti?