Save 20% off! Join our newsletter and get 20% off right away!

COLE PALMER, CHÂTEAU PALMER AKULIMBILANA ‘COLD PALMER’

Katswiri osewera mpira mu timu ya Chelsea ku magalande, Cole Palmer ali mu m’pungwem’pungwe olimbirana kulembetsa kasangalalidwe kake kotchedwa ‘Cold Palmer’ pa bwalo la khothi.

Katswiriyu yemwe ali ndi dzaka 23 dzakubadwa, anayambitsa kasangalalidweka pomwe anayamba kuchinya kwambiri zigoli pomwe akusewera mu timu ya Chelsea.

Posachedwapa Cole Palmer analembera nthambi yoteteza nzeru komanso chuma chosagwilika(Intellectual Property Office) kuti kasangalalidweka kakhale kotetezedwa ndi malamuro a dziko ndicholinga choti azitha kugwilisa ntchito potsasa katundu osiyanasiyana kuphatikizapo mowa ndi zovala.

Koma kalata yakeyi yatsusidwa ndi akatswiri opanga vinyo wa mtengo wapamwamba yemwe dzina lake ndi Château Palmer aku Bordeaux mu dziko la France.

Vinyo wa Château Palmer.

Akatswiri opanga vinyowa anapeleka chiletso chotsusana ndi ganizo la Cole Palmer lofuna kulembetsa ndikumagwilisa ntchito mawu oti ‘Cold Palmer’ makamaka pogulisa mowa chifukwa chakuti izi zintha kuwononga dzina lawo lodziwika bwino ku nkhani zopanga vinyo ‘Château Palmer’ lomwe ndilachi french ndipo limatathauza Cold Palmer muchigelezi.

Padalali pano nthambi yowona komanso kuteteza nzeru ndi chuma chosagwilika (Intellectual Property Office) laku mangalande linalandira makalata a okhuzidwa onse pa nkhaniyi ndipo ikuwunikira zokamba zambali zonse. Chigamulo chomaliza chizapelekedwa nthambiyi ikamaliza kuwunikira mbali zonse bwinobwino.

Ngati chigamulo cha nthambiyi chitazakomere katswiri wa mpira Cole Palmer ndekuti kasangalalidwe kake kotchedwa ‘Cold Palmer’ kafalikira kwambiri ndikudziwaka kwa anthu okonda mowa komanso kuma fashon a zovala ndi katundu wina wapakhomo.

Izi zili chonchi, Cole Palmer akhala akusewera mpira lero pomwe timu yake Chelsea ikukumana ndi West Ham mumasewero ake achiwiri mu mpikisano wa English Premier League.

Source : Daily Mail