Save 20% off! Join our newsletter and get 20% off right away!

Bushiri Wang’alura Apolisi, Hawks komanso Nthambi Zowona Milandu ndi Chilungamo ku South Africa.

Shepherd Bushiri wabwera poyera ndiku ng’alura akuluakulu ena a apolisi ku South Africa komanso a chitetezo otchedwa Hawks anayesa kuti amafuna atapasidwa ndalama zambiri kuti awateteze komanso kuti milandu yomwe akuzengedwa “izimirire.”

Malinga ndi Bushiri, akuluakulu awa—kuphatikiza Captain Ngobeni, Captain Rebi, ndi wina yemwe amatchedwa kuti Maritz—anawawuza kuti akufuna ndalama zokwana R12 miliyoni kuchokera kwa Bushiri ndi mkazi wake.

Ananenanso kuti mkulu wina wa Hawks, amene amangomutchula kuti “General Sibiya,” anali pakati pa zomwe zimachitikazo, ponena kuti anthu ake ena anakumana ndi general ameneyo ndipo ndalama zambiri zinkapemphedwa m’njira yokhudza dzina lake.

Hawks Police representative

Bushiri akuti zochitika zoterezi zinamukakamiza kupita kukadandaula ku IPID (Independent Police Investigative Directorate) kuti akonze ntchitoyi mwa kuwombeza akuluakuluwo ndi kuwasunga mmanja.

Koma akuti ntchitoyo inalephereka chifukwa munthu wina mkati mwa National Prosecuting Authority (NPA) anawauza akuluakuluwa ndipo zinachititsa kuti iwo omwe anakadandaula akhale otsakidwa kuphatikiza ndi mkazi wawo.

Iye akuwonjeza kuti maloya ake ku South Africa anamangidwanso ndikusungidwa kwa maola ambiri ndi a Hawks, zomwe akuti zinali njira yo lwachititsa mantha ndi kulepheretsa kufufuzidwa kwa ziphuphu mkati mwa apolisi.

Bushiri akuti pano wakhala akulandira mawu a chiwopsezo osiyanasiyana, kuphatikiza zochitika zomwe zimayika moyo wawo pachiopsyezo—zomwe zimamupatsa chikhulupiriro kuti milandu yake si nkhani yokhudza malamulo basi, koma “kuzunziridwa” chifukwa cha ziphuphu zomwe akuti zili mkati mwa thambi lowona za milandu ndi chilungamo

Source: eNCA