Save 20% off! Join our newsletter and get 20% off right away!

BAMBO WAKU DELHI WANJATIDWA KAMBA KOGWILILIRA MAYI AKE

Bambo wa dzaka 39 ku Delhi mu dziko la India ali m’chitokosi cha apolisi kamba kodzuza komanso kugwililira mayi wawo owabeleka a dzaka 65 pamene amachokera ku ulendo wa chiyero ku Saudi Arabia mwezi uno.

Nkhaniyi inadziwika pamene mchemwali wake wamkulu wa bamboyi anakamang’ala ku polisi kuti bamboyi wakhala akuchitira nkhanza komanso kugwililira mobwelezabweleza mayi awowa mwezi uno.

Malinga ndi wamkulu wa police muderali, mayiwa akuti adapita ku Saudi Arabia pa 25 July ndi amuna awo a dzaka 72 komanso mwana wawo wamkazi ku ulendo wa chiyero wa chipembezo cha aluya (pilgrimage). Mkatimkati mwa ulendowu, mwana wawo wamunayi anawayimbila lamya kudzera pa lamya ya amuna awo ndikuwawuza kuti ali ndi khalidwe loipa kotero samayenera kupita ku ulendo wa chiyero kotero pakufunika kuti bambo awo abwelere mwam’sanga ku Delhi komanso azathese banja.

Bamboyi yemwe akudziwika ndi dzina loti Md Firoz lachinsinsi Suhel akuti anachitira nkhaza mayi akewa atangofika kuchokera ku Saudi Arabia pa 11 mwezi uno. Potsatira izi, mayiwa anadzadzidwa ndi mantha ndipo anapita kukakhala kwa azilamu awo a mwana wawo wamkulu wamkazi. Koma pamene anabwelera kunyumba kwawo, bamboyi anapitiliza nkhalidwe lochitira nkhaza mayi akewa.

“Anawauza kuti akufuna awayakhule pa awiri ndipo anakawatsekera mu chipinda china ndikuwaopsyeza ndi mpeni kenako kuwagwililira,” wamkulu wa polisi adaonjezera motero.

Izi zitachitika, mayiwa sanafotokozere aliyense kamba ka manyazi koma zinapezeka kuti bamboyi anagwililiranso mayi akewa pa 14 mwezi uno(August) apa ndipamene adaganiza zowadziwitsa a polisi nkhaniyi.

“Anandikakamiza kuvula zovala zanga za chipembezo zobisa nthupi, kunditsekera mu chipinda ndikundimenya kwambiri kenako kundigwililiranso. Anawauza amuna anga kuti amandiononga pomandikonda ndikundipangila zinthu komanso kunditenga ku ulendo wa chiyero,” adatero mayi ogwililidwawo malingana ndi zomwe analemba a Hindustan Times.

Malingana ndi lipoti la apolisi, bamboyi wakhala akutsekera mayi akewa mchipinda ndikumawamenya modetsa nkhawa komanso kuwagwililira ponena kuti akuwapatsa chilango kamba ka khalidwe lawo loipa ngakhale mayiwa amamuchondelera kuti aleke izi potengera kuti ndi mayi ake.

Padakali pano kafukufuku ali mkati ndipo apolisi anamusegulira mlandu bamboyi motsatira malamulo a BNS(Bharatiya Nyaya Sanhita).

Source: Hindustan Times