Mkazi wina ku Iran, yemwe anakwatitsidwa ali ndi zaka khumi ndi ziwiri(12) ndipo wakhala ankazunzidwa kwa zaka zambiri ndi mwamuna wakeyo, tsopano ali pa chiopsyezo chophedwa ndi boma ngati atalephere kulipira ndalama zokwana 10 biliyoni tomans (pafupifupi £80,000) kwa banja la mwamuna wake pofika mwezi wa December.
Goli Kouhkan, yemwe tsopano ali ndi zaka 25, ankateteza mwana wake wamwamuna wazaka zisanu yemwe ankamenyedwa kwambiri ndi bambo ake. Tsiku lina bamboyu ali mkati momenya wamwanayo, mayiwa analowera ndikuyitana wachibale wawo ndipo nkhondo inayambika pakati pa bamboyo ndi ankolo a mkaziyo, mwangozi mwamuna wa mkaziyo anamwalira.
Koma m’malo moti alemekezedwe ngati wopulumuka pa ukwati wa msinkhu wochichepere komanso nkhanza zapakhomo, Kouhkan anamangidwa ali ndi zaka 18, ndipo anafunsidwa mafunso popanda loya, ndipo anakakamizidwa kusaina ganizo lokuti ndiwolakwa pakuti sanathe kuwerenga kamba koti ndi osaphunzira.
Malinga ndi lamulo la qisas ku Iran, moyo wake ukhoza kupulumuka ngati athe kupeza ndalama zomwe banja la mwamuna wake likufuna — zomwe n’zovuta kwambiri kupeza popeza amachokera ku banja losauka komanso lam’dera lomwe limanyozedwa.
Ngakhale atapeza ndalama, akhoza kukakamizidwa kuchoka m’dera la Gorgan ndipo palibe chitsimikizo choti adzawonanso mwana wake, yemwe pano akusamaliridwa ndi abale a mwamuna wake.
Akatswiri oyang’anira ufulu wa anthu akunena kuti nkhaniyi ikusonyeza kulephera kwa dongosolo lachilungamo ku Iran poteteza atsikana amene amakwatitsidwa adakali achichepere, komanso momwe dongosololi likupondereza ozunzidwa m'malo mowathandiza.
Source: The Guardian
Msungwana yemwe anapulumuka ku nkhaza za m'banja ali pa chiopsyezo chonyongedwa ku Iran
Mkazi wina ku Iran, yemwe anakwatitsidwa ali ndi zaka khumi ndi ziwiri(12) ndipo wakhala ankazunzidwa kwa zaka zambiri ndi mwamuna wakeyo, tsopano ali pa chiopsyezo chophedwa ndi b...
By editor·April 8, 2026·2 min read
1


More in home
homeeditor
Ancient longevity drink green tea may lower cholesterol, cut risk of early death by 16%
For centuries, green tea has been celebrated as a health-promoting drink, and modern research continues to uncover evide…
1661 1
homeeditor
Thousands of Zimbabwean, Malawian Nationals Await Repatriation as Musina Centre Faces Backlog
Processing of foreign nationals at the Musina Repatriation Centre in South Africa's Limpopo Province is continuing as au…
2907 1
homeeditor
Ebola Virus Disease returns to haunt Democratic Republic of the Congo
Just when it seemed the nightmare had faded, Ebola Virus Disease is back in the Democratic Republic of the Congo like it…
166 0


