Save 20% off! Join our newsletter and get 20% off right away!

APHA MWAMUNA WAKE POMUFINYA KUMOYO MOTHANDIZIDWA NDI MAYAKE

A polisi a m’boma la Nsanje akusunga amayi awiri powaganizira kuti anapha bambo wina wa dzaka 25. mu mudzi wa Nyale kwa Traditional Authority Mbenje.

Amayiwa omwe ndi Moreen Jambo, wa dzaka 18, ndi Modester Foster, wa dzaka 32, amachokera mmudzi wa Nyale ndipo akuganizilidwa kuti apha bambo Khefasi Liwichi, adzaka 25, omwe amachokera mmudzi wa Gamba kwa mfumu yayikulu Mbenje m’boma la Nsanje.

Utsiku wapa 31 October, bambo Khefasi adakangana kwambiri ndi mkazi wawo Moreen chifukwa adachoka pakhomopo tsiku lonse nkubwela mochedwa.

N’kanganowu udayambitsa ndewu ndipo Moreen adathawila kwa mayi ake omwe amakhala pafupi nawo. Bambo Khefasi powona izi sadayilole ndipo adapita kwa Apongozi awo konko kukayishosha bhawuthi.

Popeza Moreen ndi Mayake Modestor adali team imodzi, adamugwila mwamuna uja nkumukoka maliseche mpaka bamboyo kumwalira.

Atamutengera kuchipatala zinaziwika kuti bamboyi adamwalira kamba ka ululu womwe udaza kamba kotchosedwa maliseche.

Padakali pano amayi awiriwa akusungidwa mchitokosi cha apolisi pomwe akuyembekezera kukaonekera ku bwalo la milandu.

Nsanje Police Deputy PRO
, Constable Jabulani Ng’oma, wavomeleza za nkhani yi