Save 20% off! Join our newsletter and get 20% off right away!

Adzukulu Ku Area 18 Alandila Mphatso Za Ndalama Zoposela 5 million kwacha 🙏🏾

Thandizo la katundu osiyana wa ndalama zoposela 5 million kwacha laperekedwa lero pa 20 June kwa maanja a sanu ndi atatu (8) omwe amagwira ntchito yokumba manda aku area 18.

Izi zachitika pamene Utumiki wa Salvation for All Minstries International motsogodzedwa ndi Mtsogoleri wawo Apostle Clifford Kawinga mongwirizana komanso abusa Yassin Gama ampingo Mvama C.C.A.P. anakhudzika ndikudzipereka kwao pakugwira ntchito pamene dziko lanthu linakhudzidwa ndi mlili wa covid 19

Wina wa katundu yemwe waperekedwa ngati njira ngati imodzi yothokoza adzukuluwa pantchito yomwe anagwira, ndi njinga, nsalu, mafuta ophikira ndi ndalama zokwana MK250,000.00

Pamwambo wopereka thandizowu Akawinga ati pomwe anthu amkasalidwa ndi mliliwu anthuwa ankagwira ntchito yawo modzipereka posawerengera kuospya kwake