Save 20% off! Join our newsletter and get 20% off right away!

Mkazi wa ku Area 23 Wamangidwa Kamba Kovulaza Mwamuna Wake Ndi Madzi Otentha Poti Analemba Wantchito Wamkazi

Apolisi a ku Area 23 amanga mkazi wazaka 34, dzina lake Bernadetta Awali, chifukwa choti anawotcha mwamuna wake, Yamikani Jonasi, ndi madzi otentha pambuyo pa mkangano wokhudza kulemba mtsikana wantchito m’nyumba.

Malinga ndi apolisi, banjali lomwe lakhala pa ukwati kwa zaka zisanu ndi ziwiri, lidayamba kukangana pomwe Jonasi adanena kuti akufunika kulemba munthu wothandiza panyumba. Adanena kuti Awali akuvutika kusamalira banja Kamba koti amakhala otanganidwa ndikuchita malonda ake.

Komabe, Awali akuti anakana lingaliroli chifukwa cha mantha oti mwamuna wake angachite chikondi ndi mtsikana wothandizira ntchito nyumbayo. Mantha amenewa akuti amachokera m’mbiri ya ubale wawo, popeza Awali kale anali wogwira ntchito m’nyumba ya a Jonasi ndipo Jonasi adasiya mkazi wake wakale Kamba ka Awali.

Mkanganowu unakula kwambiri tsiku la ngoziyo, ndipo akuti Awali anayamba kumuvulaza mwamuna wake ziwalo zake zogonana kenako kumuwotcha ndi madzi otentha.

Jonasi wavutika kwambiri ndi moto womwe unamuwotcha ndipo akulandira chithandizo ku Kamuzu Central Hospital, komwe madokotala akuti ali pa ululu waukulu koma ali m’malo otetezeka.

Apolisi atsimikiza kuti Awali ali m’ndende ndipo adzazengedwa milandu akamaliza kafukufuku.