Mkazi wina ku Iran, yemwe anakwatitsidwa ali ndi zaka khumi ndi ziwiri(12) ndipo wakhala ankazunzidwa kwa zaka zambiri ndi mwamuna wakeyo, tsopano ali pa chiopsyezo chophedwa ndi boma ngati atalephere kulipira ndalama zokwana 10 biliyoni tomans (pafupifupi £80,000) kwa banja la mwamuna wake pofika mwezi wa December.
Goli Kouhkan, yemwe tsopano ali ndi zaka 25, ankateteza mwana wake wamwamuna wazaka zisanu yemwe ankamenyedwa kwambiri ndi bambo ake. Tsiku lina bamboyu ali mkati momenya wamwanayo, mayiwa analowera ndikuyitana wachibale wawo ndipo nkhondo inayambika pakati pa bamboyo ndi ankolo a mkaziyo, mwangozi mwamuna wa mkaziyo anamwalira.
Koma m’malo moti alemekezedwe ngati wopulumuka pa ukwati wa msinkhu wochichepere komanso nkhanza zapakhomo, Kouhkan anamangidwa ali ndi zaka 18, ndipo anafunsidwa mafunso popanda loya, ndipo anakakamizidwa kusaina ganizo lokuti ndiwolakwa pakuti sanathe kuwerenga kamba koti ndi osaphunzira.
Malinga ndi lamulo la qisas ku Iran, moyo wake ukhoza kupulumuka ngati athe kupeza ndalama zomwe banja la mwamuna wake likufuna — zomwe n’zovuta kwambiri kupeza popeza amachokera ku banja losauka komanso lam’dera lomwe limanyozedwa.
Ngakhale atapeza ndalama, akhoza kukakamizidwa kuchoka m’dera la Gorgan ndipo palibe chitsimikizo choti adzawonanso mwana wake, yemwe pano akusamaliridwa ndi abale a mwamuna wake.
Akatswiri oyang’anira ufulu wa anthu akunena kuti nkhaniyi ikusonyeza kulephera kwa dongosolo lachilungamo ku Iran poteteza atsikana amene amakwatitsidwa adakali achichepere, komanso momwe dongosololi likupondereza ozunzidwa m’malo mowathandiza.
Source: The Guardian
							









Leave a Reply