Save 20% off! Join our newsletter and get 20% off right away!

TRIEPHORNIA MPINJANJIRA FOUNDATION IDALITSA MSUNGWANA WOCHITA MALONDA AKAUNJIKA NDI MK3 MILLION

LILONGWE-April 18, 2025

Bungwe la Triephornia Thomson Mpinganjira Foundation lachisanu loyera pa 18 April 2025 ladalitsa msungwana Monalisa Memory Mandala yemwe amachiira malonda azovala za kaunjika ku Area 18, mu mzinda wa Lilongwe.

Thandizoli ladza potsatila chidwi chomwe mkulu wa bungweli Triephornia Mpinganjira anawona patsamba la mchezo la Tiktok pomwe msungwanayu analemba uthenga wowonetsa kuthodwa ndi buzinezi yake omwenso unali mbali imodzi yotsatsa malonda komanso kulimbikitsa achinyamata kusafooka pa buzinezi.

Mayi Mpinganjira atawona uthenga, anamulonjeza Monalisa kuti amuthandiza pomuwonjezera mpamba wa buzinezi yake kuti ukule ncholinga choti adzathandizenso ena kutsogoloku.

Atalandira nthandizo landalamayi ku Area 18, Monalisa anali wodzidzimutsidwa ponena kuti sanayembekezere kuti angadalitsike motere.

Imyeyu anati nthandizoli labwera munthawi yake pomwe wakhala alulingalira njira zina zomwe zingapolititsire patsogolo businezi yake koma vuto unali mpamba wowonjezera.

Mandala anati buzinezi yake yakhale ikuyenda mwapendapenda kuyambila mchacha cha 2021.

“Ndinayamba buzineziyi mtagulitsa zovala zanga zanthupi zomwe zimkangokhala ndi MK15,300. Ndinayamba mtangomaliza sukulu yanga ya ukachenjede ku DMI pa maphunziro Social Work.

“Nditapanga graduation mchaka cha 2022, poti mwayi wachintchito panalibe ndinalimbikira businezi mpakana pano ncholinga choti ndidzikwaniritsa zosowa zanga pamoyo”, anatero Memory yemwe ali ndi zaka 26.

Mandala anayamika bungweli pofikira achinyama, amayi ochepekedwa mu buzinezi.

“Anandiyimbira phone mmodzi mwa akuluakulu ku bungweli kuti adziwe zambiri za buzinezi yanga ncholinga choti ndithandizidwe, sindinakhulupirire kufikira leroli pomwe abweradi kudzandipatsa ndalamayi.

“Ndikuthokoza kwambiri utsogoloreli wabungweli motsogozedwa ndi MadamTriphoniaMpinganjira kuti chakuta apitirize kuwapatsa zochuluka ncholinga choti akafikirenso ena. Ndalamayi ndigulira ma bail atatu pazovala zomwe amazifuna makasitomala anga”.

Imyeyu analangiza achinyama kuti adzigwiritsa bwino ntchito masamba amchezo pa zinthu zothandiza.

Mmawu ake, nthumwi ya bungweli a Wezi Chiweta anati ndicholinga cha bungweli kusitha miyoyo ya Malawi ncholinga choti adzidzidalira pachuma.

Chiweta anawonjezera kuti bungweli linakhudzidwa ndi msungwanayu yemwe sanapeze ntchito atamaliza sukulu koma akulimbikira pa buzineni.

A Chiweta anawonjezera kuti bungweli liyesetsa kufikira achinyamata ndi amayi womwe alindikuthekera kuti moyo wawo upite patsogolo powathandiza ndi zipangizo kapena ndalama pa ntchito zamanja ndi buzinezi

Bungweli linkhazikitsidwa ndi Madam Dr Triephornia Mpinjanjira ndicholinga chofuna kuthandiza anthu mdziko muno mmagawo a buzinezi, ntchito zamanja, sukulu kuti azidzidalira pa chuma.