Save 20% off! Join our newsletter and get 20% off right away!

MAYI ALILA ATATENGA MIMBA YOTI SIYAKE

Yalakwa Ku Australia. Mayi wina anapita ku chipatala cha Monash IVF kuti athe kutenga mimba kudzera mu njira ya sayansi. Imene amamuyika embryo mu mimba.

Zinthu zinali bwino mpaka poti anatenga mimba.

Koma mbola ! Embryo imene adamuyika mu mimba mayiyu si ya mwana wake!

Ena akuti chipatala chinaphatikiza ma embryo molakwika – ndiye mwana uja anali wa banja lina osati la mkazi uja.

Nthawi itapita, mwana anabadwa ali bwino, koma mayi uja powona ali “Nooooo! Uyu si mwana wanga”. Mzungu ubeleka bwanji Chinese ?

Mpaka chipatala chitayeza DNA chapezadi kuti mwana anabadwitsa mayiyo si wawodi.

CEO wa chipatalacho wayesesa kupepesa kuti izi sizizachitikanso ndipo akaka nkoyamba koma Mayiyu wangokhala okhumudwa.

Couple ina imene Embryo idali yawo awafikila kuwawuza zoti mayi wina wabadwitsa mwana wawo koma nawo angokhala otutumuka