Save 20% off! Join our newsletter and get 20% off right away!

KUTCHONA SIKUFUNA :- NAFE TIMAFUNA TITABWELA KUMUDZI KOMA…

Pomwe Amalawi ambiri akuyesayesa kupeza mwayi woti atuluke Malawi ndikumakagwira maganyu kumaiko ena, Amalawi ena omwe ali m’maiko monga South Africa adandaula kuti ngakhale anthu ambiri amaona ngati moyo kumaiko akunja ndiwofewa izi sizili chomwechi poti amankhala akukumana ndimavuto osiyanasiyana ndipo pena akakhala amalakalaka zobwelera ku Malawi kuno koma Kamba ka mavuto amayendedwe amangokhalabe komweko.

Mmodzi mwa anthu omwe akukhala mdziko la South Africa ndipo akugwira ma ganyu osiyanasiyana wati moyo ku Jubeki ndiwovuta popeza amakhala akugwira ntchito masana ndi madzulo kuti mwina azitha kupeza ndalama ya zakudya komanso malo ogona koma chachikulu ndichakuti kangachepe kamene amasunga ndikomwe amapezeka watumiza kumudzi kwa azibale ndipo pakutha pa zonse amakhala alibenso ndalama.

Iyenso wati amalawi ena akuvutika kwambiri pachifukwa choti ma ganyu si ntchito yodalilika, lero ugwira mawa aikapo nzako ukachedwa. Pachifukwa chimenechi, amalawi ena akumatenga zinthu monga nyemba, bonya,mtedza komanso chinagwa kuti azikadya akafika ku South Africa kwinaku akusakasaka manganyu.

Iye wati ndizovuta kuti munthu uthe kumasunga ndalama kuti uzapeze poyambila ukabwerako ku Theba poti ndalama akasunga zikumathela kuthandiza abale omwe anasala ku Malawi komanso ma banja awo ndipo dzimawavuta ngakhale kubwera kumudzi nthawi ya chikondwelero cha kubadwa kwa Yesu.

“Anthu ngati ife odalira maganyu ndalama zathu zonse zikumathera kuthandiza abale ku Malawi. Olo tikati tipange plan yoti tibwere December, umva kumudzi wina wameza khasu pakufunika ndalama, Basitu yonse ya transport kulowa.” Adatero, nyamata yemwe anati dzina lake ndi Chekwere.